Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 20:4-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Koma Abimeleke sanayandikire naye; ndipo anati, Ambuye, kodi mudzaphanso mtundu wolungama?

5. Kodi iye sanati kwa ine, Ndiye mlongo wanga: ndipo mkazi iye yekha anati, iye ndiye mlongo wanga: ndi mtima wanga wangwiro ndi manja anga osacimwa ndacita ine ici.

6. Ndipo Mulungu anati kwa iye m'kulota, lode ndidziwa ine, kuti wacita ico ndi mtima wangwiro, ndipo lnenso ndinakuletsa iwe kuti usandicimwire ine: cifukwa cace sindinakuloleza iwe kuti umkhudze mkaziyo.

7. Tsopano, umbwezere munthuyo mkazi wace; cifukwa iye ndiye mneneri, ndipo adzakupempherera iwe, ndipo udzakhala ndi moyo: koma ukaleka kumbwezera, udziwe kuti udzafa ndithu, iwe ndi onse amene uli nao.

8. Ndipo Abimeleke analawira m'mamawa, naitana anyamata ace onse, nanena zonse rimenezo m'makutu mwao, ndipo anthu anaopa kwambiri.

9. Ndipo Abimeleke anaitana Abrahamu, nati kwa iye, Waticitira ife ciani iwe? Ndakucimwiranji iwe kuti waufikitsa pa ine ndi pa ufumu wanga ucimo waukuru? Wandicitira ine zosayenera kuzicita.

10. Ndipo Abimeleke anati kwa Abrahamu, Unaona ciani iwe kuti wacita ici?

11. Ndipo Abrahamu anati, Cifukwa ndinati, Pompano palibe ndithu kumuopa Mulungu, ndipo adzandipha ine cifukwa ca mkazi wanga.

12. Koma ndiye mlongo wanga ndithu, mwana wa atate wanga, koma si mwana wa amai wanga: ndipo anakhala ndi ine mkazi wanga.

13. Ndipo panali pamene Mulungu anandiyendetsa ine kunyumba kwa atate wanga, ndinati kwa mkaziyo, Ici ndico cokoma mtima udzandicitire ine, konse kumene tidzafika ife, uzinena za ine, iye ndiye mlongo wanga.

14. Ndipo Abimeleke anatenga nkhosa ndi ng'ombe nd akapolo ndi adzakazi nampatsa Abrahamu, nambwezera iye Sara mkazi wace.

Werengani mutu wathunthu Genesis 20