Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 19:8-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Taonanitu, ndiri ndi ana akazi awiri, amene sanadziwe mwamuna; ndiwaturutsire iwo kwa inu, mucite nao comwe cikomera inu; koma anthu awa musawacitire iwo kanthu; cifukwa kuti anadza iwo pansi pa mthunzi wa cindwi langa,

9. Ndipo anati iwo, Baima; natinso, Uyu anadza kuno kukhala ngati mlendo, ndipo afuna kutilamulira; tsopano tidzakucitira iwe koipa koposa iwo. Ndipo iwo anamkakamiza munthuyo Loti ndithu, nayandikira kuti aswe citseko.

10. Komo anthu aja anaturutsa dzanja lao, namlowetsa Loti momwe anali iwo m'nyumba, natseka pakhomo,

11. Ndipo anacititsa khungu m'maso mwa anthu amene anali pakhomo pa nyumba, ang'ono ndi akuru, ndipo anabvutika kufufuza pakhomo.

12. Ndipo anthu aja anati kwa Loti, Kodi muli nao ena pano? Mkamwini, ndi ana ako amuna, ndi ana ako akazi, ndi onse ali nao m'mudzi muno, uturuke nao m'malo muno:

13. popeza ife tidzaononga malo ano, cifukwa kulira kwao kwakula pamaso pa Yehova, ndipo Yehova anatitumiza ife kuti tiuononge.

Werengani mutu wathunthu Genesis 19