Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 17:3-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Ndipo Abramu anagwa nkhope pansi, ndipo Yehova ananena naye kuti,

4. Koma Ine, taona, pangano langa liri ndi iwe, ndipo udzakhala iwe atate wa khamu la mitundu.

5. Sudzachedwanso dzina lako Abramu, koma dzina lako lidzakhala Abrahamu; cifukwa kuti ndakuyesa iwe atate wa khamu la mitundu.

6. Ndipo ndikubalitsa iwe ndithu, ndipo ndidzakuyesa iwe mitundu, ndipo mafumu adzaturuka mwa iwe.

7. Ndipo ndidzalimbitsa pangano langa ndi Ine ndi iwe pa mbeu zako za pambuyo pako m'mibadwo yao, kuti likhale pangano la nthawi zonse, kuti ndikhale Mulungu wako ndi wa mbeu zako za pambuyo pako.

8. Ndipo ndidzakupatsa iwe ndi mbeu zako za pambuyo pako, dziko la maulendo anu, dziko lonse la Kanani likhale lako nthawi zonse: ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wao.

9. Ndipo Mulungu anati kwa Abrahamu, Koma iwe, uzikumbukira pangano langa, iwe ndi mbeu zako za pambuyo pako m'mibadwo yao.

10. Ili ndi pangano langa limene uzisunga pakati pa Ine ndi iwe ndi mbeu zako zapambuyo pako: azidulidwa amuna onse a mwa inu.

11. Muzidula khungu lanu; ndipo cidzakhala cizindikiro ca pangano pakati pa Ine ndi inu.

12. A masiku asanu ndi atatu azidulidwa mwa inu, ana amuna onse m'mibadwo mwanu, amene abadwa m'nyumba ndi amene agulidwa ndi ndalama kwa alendo ali onse, wosakhala mwa mbeu zako.

13. Azidulidwatu amene abadwa m'nyumba mwako ndi amene agulidwa ndi ndalama zako: ndipo pangano langa lidzakhala m'thupi mwako pangano losatha.

14. Ndipo mwamuna wosadulidwa, wosadulidwa khungu lace munthuyo amsadze mwa anthu a mtundu wace; waphwanya pangano langa.

Werengani mutu wathunthu Genesis 17