Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 16:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Sarai mkazi wace wa Abramu sanambalire iye mwana; ndipo anali ndi mdzakazi, wa ku Aigupto, dzina lace Hagara.

2. Ndipo Sarai anati kwa Abramu, Taonanitu, Yehova anandiletsa ine kuti ndisabale: lowanitu kwa mdzakazi wanga; kapena ndikalandire ndi iye ana. Ndipo Abramu anamvera mau a Sarai.

3. Ndipo Sarai mkazi wace wa Abramu anatenga Hagara mdzakazi wace wa ku Aigupto, Abramu atakhala m'dziko la Kanani zaka khumi, nampereka iye kwa Abramu mwamuna wace, kuti akhale mkazi wace.

4. Ndipo analowa kwa Hagara, ndipo iye anatenga pakati. Pamene anaona kuti anatenga pakati, anapeputsa wakuka wace m'maso mwace.

5. Ndipo Sarai anati kwa Abramu, Kusauka kwanga kukhale pa iwe: ndakupatsa iwe mdzakazi wanga pamtima pako; ndipo pakuona kuti anatenga pakati anandipeputsa ine m'maso mwace: Yehova aweruze pakati pa iwe ndi ine.

6. Koma Abramu anati kwa Sarai, Taona, mdzakazi wako ali m'dzanja lako, umcitire iye cimene cikukomera m'maso mwako. Ndipo Sarai anamsautsa iye, ndipo anathawa kumaso kwace.

7. Ndipo mthenga wa Yehova anampeza iye pa kasupe wa madzi m'cipululu, pa kasupe wa pa njira ya ku Suri.

8. Ndipo anati, Hagara, mdzakazi wace wa Sarai, ufumira kuti? Unka kuti? Ndipo anati, Ndithawa ine kumaso kwace kwa wakuka wanga Sarai.

9. Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa iye, Bwera kwa wakuka wako, udzicepetse wekha pamanja pace.

Werengani mutu wathunthu Genesis 16