Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 14:5-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Caka cakhumi ndicinai ndipo anadza Kedorelaomere ndi mafumu amene anali naye, nawakantha Arefai m'Aseteroti-kamaimu, ndi Azuzi m'Hamu, ndi Aemi m'Savekiriataimu,

6. ndi Ahori pa phiri lao Seiri kufikira ku Eliparana, kumene kuli pacipululu.

7. Ndipo anabwera nafika ku Eni-Misipati (ku meneko ndi ku Kadese), nakantha dziko lonse la Aamaleki, ndiponse Aamori amene akhala m'Hazezoni-tamara.

8. Ndipo anaturuka mfumu ya Sodomu, ndi ya Gomora, ndi mfumu ya Adima, ndi mfumu ya Zeboimu, ndi mfumu ya Bela (kumeneko ndi ku Zoari) ndipo anawathira nkhondo m'cigwa ca Sidimu

9. ndi Kedorelaomere mfumu ya Elamu, ndi Tidala mfumu ya Goimu ndi Amarafele mfumu ya Sinara, ndi Arioki mfumu ya Elasara; mafumu anai kugwirana ndi asanu.

10. Cigwa ca Sidimu cinali ndi zitengetenge tho; ndipo anathawa mafumu a ku Sodomu ndi Gomora nagwa m'menemo: amene anatsala anathawira kuphiri.

11. Ndipo anatenga cuma conse ca Sodomu ndi Gomora ndi zakudya zao zonse, namuka.

12. Ndipo anagwira Loti mwana wa Abramu amene anakhala m'Sodomu, ndi cuma cace, namuka.

13. Ndipo anadza wina amene anapulumuka namuuza Abramu Mhebri; ndipo iye analinkukhala pa mitengo yathundu ya pa Mamre M-amori, mkuru wace wa Esakolo, ndi mkuru wace wa Aneri; amenewo ndiwo opangana naye Abramu.

14. Pamene anamva Abramu kuti mphwace anagwidwa, anaturuka natsogolera anyamata ace opangika, obadwa kunyumba kwace, mazana atatu kudza khumi ndi asanu ndi atatu, nawalondola kutikira ku Dani.

15. Ndipo anadzigawanizira iwo usiku, iye ndi anyamata ace, nawakantha, nawapitikitsa kufikira ku Hoba, ndiko ku dzanja lamanzere la ku Damasiko.

16. Ndipo anabwera naco cuma conse, nabwera naye Loti yemwe ndi cuma cace, ndi akazi ndi anthu omwe.

17. Ndipo anaturuka mfumu ya Sodomu kukomana naye, atabwera anatha kuwakantha Kedorelaomere ndi mafumu amene anali naye, ku cigwa ca Save (ndiko ku cigwa ca mfumu),

18. Ndipo Melikizedeke mfumu ya ku Salemu, anaturuka nao mkate ndi vinyo: iye ndiye wansembe wa Mulungu Wamkurukuru.

Werengani mutu wathunthu Genesis 14