Ndipo anadza wina amene anapulumuka namuuza Abramu Mhebri; ndipo iye analinkukhala pa mitengo yathundu ya pa Mamre M-amori, mkuru wace wa Esakolo, ndi mkuru wace wa Aneri; amenewo ndiwo opangana naye Abramu.