Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 1:26-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

26. Ndipo anati Mulungu, Tipange munthu m'cifanizo cathu, monga mwa cikhalidwe cathu: alamulire pa nsomba za m'nyanja, ndi pa mbalame za m'mlengalenga, ndi pa ng'ombe, ndi pa dziko lonse lapansi, ndi pa zokwawa zonse zakukwawa pa dziko lapansi.

27. Mulungu ndipo adalenga munthu m'cifanizo cace, m'cifanizo ca Mulungu adamlenga iye; adalenga iwo mwamuna ndi mkazi.

28. Mulungu ndipo anadalitsa iwo, ndipo adati kwa iwo, Mubalane, mucuruke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pa nsomba za m'nyanja, ndi pa mbalame za m'mlengalenga, ndi pa zamoyo zonse zakukwawa pa dziko lapansi.

29. Ndipo anati Mulungu, Taonani, ndakupatsani inu therere lonse lakubala mbeu liri pa dziko lapansi, ndi mitengo yonse m'mene muli cipatso ca mtengo wakubala mbeu; cidzakhala cakudya ca inu:

30. ndiponso ndapatsa zinyama zonse za dziko lapansi, ndi mbalame zonse za m'mlengalenga, ndi zakukwawa zonse za dziko lapansi m'mene muli moyo, therere laliwisi lonse likhale cakudya: ndipo kunatero.

31. Ndipo anaziona Mulungu zonse zimene adazipanga, ndipo, taonani, zinali zabwino ndithu. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lacisanu ndi cimodzi.

Werengani mutu wathunthu Genesis 1