Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 6:5-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Ndipo ndidzaika mitembo ya ana a Israyeli pamaso pa mafano anu, ndi kumwaza mafupa anu mozungulira maguwa anu a nsembe.

6. Pokhala inu ponse midzi idzapasuka, ndi misanje idzakhala yabwinja; kuti maguwa anu a nsembe akhale opasuka ndi mabwinja, ndi mafano anu asweke nalekeke, ndi zoimiritsa zanu zadzuwa zilikhidwe, ndi nchito zanu zifafanizidwe.

7. Ndi ophedwa adzagwa pakati panu, matero mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

8. Koma ndidzasiyapo otsala, popeza mudzakhala nao ena akupulumuka lupanga mwa amitundu pobalalitsidwa inu m'maiko maiko.

9. Pamenepo akupulumuka anu adzandikumbukila Ine kwa amitundu kumene anatengedwa ndende, kuti ndasweka ndi mtima wao wacigololo wolekana ndi Ine, ndi maso ao acigololo akutsata mafano ao; ndipo iwo adzakhala onyansa pamaso pao pa iwo eni, cifukwa ca zoipa anazicita m'zonyansa zao zonse.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 6