Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 6:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo mau a Yehova anandidzera, kuti,

2. Wobadwa ndi munthu iwe, lozetsa nkhope yako ku mapiri a Israyeli, uwanenere,

3. nunene, Mapiri a Israyeli inu, tamverani mau a Yehova Mulungu: Atero Yehova Mulungu kwa mapiri ndi zitunda, kwa mitsinje ndi zigwa, Taonani, Ine ndikufikitsirani lupanga, ndipo ndidzaononga misanje yanu.

4. Ndi maguwa anu a nsembe adzakhala opasuka, ndi zoimiritsa zanu zadzuwa zidzasweka; ndipo ndidzagwetsa ophedwa anu pamaso pa mafano anu.

5. Ndipo ndidzaika mitembo ya ana a Israyeli pamaso pa mafano anu, ndi kumwaza mafupa anu mozungulira maguwa anu a nsembe.

6. Pokhala inu ponse midzi idzapasuka, ndi misanje idzakhala yabwinja; kuti maguwa anu a nsembe akhale opasuka ndi mabwinja, ndi mafano anu asweke nalekeke, ndi zoimiritsa zanu zadzuwa zilikhidwe, ndi nchito zanu zifafanizidwe.

7. Ndi ophedwa adzagwa pakati panu, matero mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 6