Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 44:19-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Ndipo akaturukira ku bwalo lakunja, ku bwalo lakunja kuti anthu, azibvula zobvala zao zimene atumikira nazo, naziike m'zipinda zopatulika, nabvale zobvala zina; angapatule anthu ndi zovala zao.

20. Ndipo asamete mitu yao, kapena asalekerere nzera za tsitsi lao zikule, azingosenga mitu yao.

21. Kungakhale kumwa vinyo, wansembe asamwe polowa ku bwalo la m'katimo.

22. Kungakhale kutenga amasiye kapena osudzulidwa akhale akazi ao, asacite; koma atenge anamwali a mbeu ya nyumba ya Israyeli, kapena wamasiye ndiye wamasiye wa wansembe.

23. Ndipo aziphunzitsa anthu anga asiyanitse pakati pa zopatulika ndi zinthu wamba, ndi kuwazindikiritsa pakati pa zodetsa ndi zoyera.

24. Ndipo pakakhala mlandu, aimeko kuweruza; auweruze monga mwa maweruzo anga, ndipo azisunga malamulo anga, ndi malemba anga, pa madyerero anga onse oikika; napatulikitse masabata anga.

25. Ndipo asayandikire kwa munthu ali yense wakufa, angadzidetse; koma cifukwa ca atate, kapena mai, kapena mwana wamwamuna, kapena mwana wamkazi, kapena mbale, kapena mlongo wopanda mwamuna, nkuloleka kudzidetsa.

26. Ndipo atayeretsedwa amwerengere masiku asanu ndi awiri.

27. Ndipo tsiku loti alowa m'malo opatulika, bwalo lam'kati, kutumikira m'malo opatulika, apereke nsembe yace yaucimo, ati Ambuye Yehova.

28. Ndipo adzakhala naco colowa; Ine ndine colowa cao; musawapatsa colandira cao m'Israyeli; Ine ndine colandira cao.

29. Azidya nsembe yaufa, ndi nsembe yaucimo, ndi nsembe yoparamula; ndipo ziri zonse zoperekedwa ciperekere m'Israyeli ndi zao.

30. Ndi zoyamba za zipatso zoyamba za zinthu ziri zonse, ndi nsembe za kweza ziri zonse za nsembe zanu zonse zokweza nza ansembe; muperekenso ufa wanu woyamba kwa wansembe, kuti mdalitso ukhalebe pa nyumba yako.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 44