Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 44:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pamenepo anandibweza njira ya ku cipata cakunja ca malo opatulika coloza kum'mawa, koma cinatsekedwa.

2. Ndipo Yehova anati kwa ine, Cipata ici citsekeke, cisatseguke, osalowako munthu; pakuti Yehova Mulungu wa Israyeli walowerapo; cifukwa cace citsekeke.

3. Koma kunena za kalonga, iye akhale m'menemo monga kalonga kudya mkate pamaso pa Yehova; alowe ku njira ya ku khonde la cipata, naturukire njira yomweyi.

4. Atatero anamuka nane njira ya cipata ca kumpoto kukhomo kwa kacisi, ndipo ndinapenya, taonani, ulemerero wa Yehova unadzaza nyumba ya Yehova; pamenepo ndinagwa nkhope pansi.

5. Ndipo Yehova anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, samalira bwino, nupenye ndi maso ako, numve m'makutu mwako zonse ndidzanena nawe, kunena za malemba onse a nyumba ya Yehova, ndi malamulo ace onse; nusamalire bwino malowedwe a nyumbayi, ndi maturukidwe ace onse a malo opatulika.

6. Nunene kwa opandukawo, kwa nyumba ya Israyeli, Atero Ambuye Yehova, Nyumba ya Israyeli inu, Zikukoleni zonyansa zanu zonse;

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 44