Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 42:11-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Ndipo njira ya pakhomo pao inanga maonekedwe a njira ya ku nyumba yazipinda yoloza kumpoto, inalingana nayo m'litali mwace, momwemonso kupingasa kwace; ndi m'maturukiro mwace monse munali monga mwa macitidwe a inzace, ndi monga mwa makomo a inzace.

12. Ndi monga mwa makomo a zipinda za kumwela panali khomo polekeza njira, ndiyo njira yokhudzana ndi linga la kum'mawa polowamo.

13. Pamenepo anati kwa ine, Zipinda za kumpoto, ndi zipinda za kumwela, ziri cakuno ca mpatawo, ndizo zipinda zopatulika, kumene ansembe okhala pafupi pa Yehova azidyera zinthu zopatulikitsa; kumeneko aziika zopatulikitsa, ndi nsembe yaufa, ndi nsembe yaucimo, ndi nsembe yoparamula; pakuti malowo ndi opatulika.

14. Atalowa ansembe asaturukenso m'malo opatulika kumka ku bwalo lakunja, koma komweko aziika zobvala zao zimene atumikira nazo; pakuti ziri zopatulika; ndipo abvale zobvala zina, nayandikire zinthu wamba za anthu.

15. Atatha tsono kuyesa nyumba ya m'katimo, anaturuka nane njira ya cipata coloza kum'mawa, nayesa bwalo pozungulira pace.

16. Anayesa mbali ya kum'mawa ndi bango loyesera, mabango mazana asanu, kuyesa ndi bango loyesera, pozungulira pace.

17. Anayesa mbali ya kumpoto mabango mazana asanu, kuyesa ndi bango loyesera, pozungulira pace.

18. Anayesa mbali ya kumwela mabango mazana asanu, kuyesa ndi bango loyesera,

19. Anatembenukira ku mbali ya kumadzulo, nayesa mabango mazana asanu ndi bango loyesera.

20. Analiyesa mbali zace zinai, linali nalo linga pozungulira pace, utali wace mazana asanu, citando cace mazana asanu, kusiyanitsa pakati pa zopatulika ndi zawamba.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 42