Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 40:9-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Pamenepo anayesa khonde la kucipata mikono isanu ndi itatu, ndi mphuthu zace mikono iwiri; ndi khonde la kucipata linaloza kukacisi.

10. Ndi zipinda za alonda za ku cipata ca kum'mawa ndizo zitatu cakuno, ndi zitatu cauko, zitatuzi nza muyeso umodzimodzi, ndi mphuthuzo nza muyeso umodzimodzi, cakuno ndi cauko.

11. Ndipo anayesa kupingasa kwa cipata pakhoma pace mikono khumi, ndi utali wace wa cipata mikono khumi ndi itatu;

12. ndi pakhomo pa zipinda za alonda panali kakhoma ka mkono umodzi cakuno, ndi kakhoma ka mkono umodzi cauko; ndi zipinda za alonda mikono isanu ndi umodzi cakuno, ndi mikono isanu ndi umodzi cauko.

13. Ndipo anayesa cipata kuyambira ku tsindwi la cipinda ca alonda cimodzi, kufikira ku tsindwi la cinzace, kupingasa kwace ndiko mikono makumi awiri ndi isanu; makomo napenyana.

14. Anamanganso nsaaamira za mikono makumi asanu ndi limodzi; ndi bwalo la pakati pa cipata lidafikira kunsanamira.

15. Ndipo kuyambira pa khomo lolowera la cipata kufikira khomo la khonde la cipata m'katimo ndiko mikono makumi asanu.

16. Ndipo panali mazenera a made okhazikika pazipinda ndi m'makhoma a pakati pao, m'kati mwa cipata pozungulira ponse; momwemonso pazidundumwa; ndipo panali mazenera pozungulira ponse m'katimo, pa nsanamirazo panali akanjedza.

17. Pamenepo analowa nane ku bwalo lakunja, ndipo taonani, panali zipinda, ndi moyalidwa miyala mokonzekera bwalo pozungulira ponse; moyalidwa miyalamo munali zipinda makumi atatu.

18. Ndipo moyalidwamo munali pa mbali ya zipata molingana ndi utali wace wa zipata, ndimo moyalidwa mwamunsi.

19. Pamenepo anayesa kupingasa kwace kuyambira pakhomo pace pacipata cakunsi, kufikira kumaso kwace kwa bwalo la m'kati kunja kwace, mikono zana kum'mawa, ndi kumpoto.

20. Ndi cipata ca bwalo lakunja coloza kumpoto anaciyesa m'litali mwace, ndi kupingasa kwace.

21. Ndi zipinda zace ndizo zitatu cakuno, ndi zitatu cauko, ndi makhoma a pakati pace; ndi zidundumwa zace zinali monga mwa muyeso wa cipata coyambaco, m'litali mwace mikono makumi asanu, ndi kupingasa kwace mikono makumi awiri mphambu isanu.

22. Ndi mazenera ace, ndi zidundumwa zace, ndi akanjedza ace, anali monga mwa muyeso wa cipata coloza kum'mawa; ndipo anakwerako ndi makwerero asanu ndi awiri, ndi zidundumwa zace zinali pakhomo.

23. Ndipo panali cipata ca bwalo lam'kati, copenyana ndi cipata cinzace cakunja kumpoto, ndi ca kum'mawa; ndipo anayesa kuyambira kucipata kufikira kucipata mikono zana.

24. Ndipo ananditsogolera kumka kumwela, ndipo taonani, panali cipata kumwela, nayesa makhoma a pakati pace, ndi zidundumwa zace, monga mwa miyeso yomweyi.

25. Ndimo munali mazenera m'menemo, ndi m'zidundumwa zace pozungulirapo, monga mazenera ena aja, m'litali mwace mikono makumi asanu, ndi kupingasa kwace mikono makumi awiri mphambu isanu.

26. Ndipo panali makwerero asanu ndi awiri okwererapo, ndi zidundumwa zace kumaso kwace; ndi pa nsanamira zace cakuno ndi cauko panali akanjedza.

27. Ndipo panali cipata ca bwalo lam'kati cakulozakumwela, nayesa kuyambira kucipata kufikira kucipata kumwela mikono zana.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 40