Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 40:40-49 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

40. Ndi ku mbali yina ya khonde kunja, pakukwerera polowera pa cipata ca kumpoto, kunali magome awiri, ndi ku mbali inzace ya kucipata kunali magome awiri.

41. Magome anai cakuno, ndi magome anai cauko, ku mbali ya cipata; magome asanu ndi atatu, amene anapherapo nsembe.

42. Ndipo panali magome anai a nsembe yopsereza a miyala yosema, m'litali mwace mkono ndi nusu, kupingasa kwace mkono ndi nusu, msinkhu wace mkono umodzi; pamenepo adafoika zipangizo zimene anaphera nazo nsembe yopsereza ndi nsembe yophera.

43. Ndi ziciri zangowe, cikhato m'litali mwace, zinamangika m'katimo pozungulirapo; ndi pamagome panali nyama ya nsembe.

44. Ndi kunja kwa cipata ca m'kati kunali tinyumba ta oyimba m'bwalo lam'kati, ku mbali ya cipata ca kumpoto; ndipo tinaloza kumwela, kena ku mbali ya cipata ca kum'mawa kanaloza kumpoto.

45. Ndipo anati kwa ine, Kanyumba aka koloza kumwela nka ansembe odikira kacisi.

46. Ndi kanyumba koloza kumpoto nka ansembe odikira guwa la nsembe, ndiwo ana a Zadoki amene ayandikira kwa Yehova mwa ana a Levi, kumtumikira Iye.

47. Ndipo anayesa bwalolo mikono zana m'litali mwace, ndi mikono zana kupingasa kwace, lamphwamphwa; ndi guwa la nsembe linali kukhomo kwa nyumba.

48. Pamenepo anadza nane ku khonde la kacisi, nayesa mphuthu za khonde, mikono isanu cakuno, ndi mikono isanu cauko; ndi kupingasa kwa cipata, mikono itatu cakuno, ndi mikono itatu cauko.

49. M'litali mwace mwa khonde mikono makumi awiri, ndi kupingasa kwace mikono khumi ndi umodzi; ndipo panali makwerero khumi okwerera kumeneko; ndipo panali zoimiritsa pa nsanamirazo, imodzi cakuno, ndi imodzi cauko.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 40