Pamenepo anadza nane ku khonde la kacisi, nayesa mphuthu za khonde, mikono isanu cakuno, ndi mikono isanu cauko; ndi kupingasa kwa cipata, mikono itatu cakuno, ndi mikono itatu cauko.