Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 32:16-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Iyi ndi nyimbo ya maliro adzalira nayo, ana akazi a amitundu adzacita nayo maliro; adzalirira nayo Aigupto ndi aunyinji ace onse, ati Ambuye Yehova.

17. Kunalinso caka cakhumi ndi ciwiri, tsiku lakhumi ndi cisanu la mwezi, anandidzera mau a Yehova, ndi kuti,

18. Wobadwa ndi munthu iwe, lirira aunyinji a Aigupto, nuwagwetsere iye ndi ana akazi a amitundu omveka kunsi kwa dziko, pamodzi ndi iwo akutsikira kudzenje.

19. Uposa yani m'kukoma kwako? tsika, nuikidwe ndi osadulidwa.

20. Adzagwa pakati pa iwo ophedwa ndi lupanga, operekedwa kwa lupanga, mkokereko ndi aunyinji ace onse.

21. Amphamvu oposa ali m'kati mwa manda adzanena naye, pamodzi ndi othandiza ace, Anatsikira, agonako osadulidwawo, ophedwa ndi lupanga,

22. Asuri ali komwe ndi msonkhano wace wonse, manda ace amzinga; ophedwa onsewo, adagwa ndi lupanga;

23. manda ao aikidwa ku malekezero a dzenje, ndi gulu lace lizinga manda ace; ophedwa onsewo adagwa ndi lupanga, amene anaopsetsa m'dziko la amoyo.

24. Elamu ali komwe ndi gulu lace lonse lozinga manda ace; ophedwa onsewo, adagwa ndi lupanga; amene anatsikira osadulidwa kunsi kwace kwa dziko, amene anaopsetsa m'dziko la amoyo, nasenza manyazi ao, pamodzi ndi iwo akutsikira kudzenje.

25. Pakati pa ophedwa anamuikira kama, iye ndi aunyinji ace onse, manda ace amzinga, onsewo osadulidwa, ophedwa ndi lupanga, pakuti anaopsetsa m'dziko la amoyo, nasenza manyazi ao, pamodzi ndi iwo akutsikira kudzenje, aikidwa pakati pa ophedwa,

26. Meseke, Tubala, ndi aunyinji ace onse ali komweko, manda ace amzinga; onsewo osadulidwa, ophedwa ndi lupanga; pakuti anaopsetsa m'dziko la amoyo.

27. Koma sagona pamodzi ndi amphamvu osadulidwa adagwawo amene anatsikira kumanda ndi zida zao za nkhondo, amene anawatsamiritsa malupanga ao; ndi mphulupulu zao ziri pa mafupa ao; pakuti anaopsetsa amphamvu m'dziko la amoyo.

28. Ndipo udzatyoledwa pakati pa osadulidwa, nudzagona pamodzi ndi iwo ophedwa ndi lupanga.

29. Edomu ali komwe, mafumu ace ndi akalonga ace onse, amene anaikidwa mu mphamvu yao, pamodzi ndi iwo ophedwa ndi lupanga; agona pamodzi ndi osadulidwa, ndi iwo akutsikira kudzenje.

30. Akalonga a kumpoto ali komwe onsewo, ndi Azidoni onse, amene anatsikira pamodzi ndi ophedwa, nacita manyazi cifukwa ca kuopsetsa anacititsaku ndi mphamvu yao, nagona osadulidwa pamodzi ndi iwo ophedwa ndi lupanga, nasenza manyazi ao pamodzi ndi iwo otsikira kudzenje.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 32