Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 28:16-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Mwa kucuruka kwa malonda ako anakudzaza m'kati mwako ndi ciwawa, ndipo unacimwa; cifukwa cace ndinakukankha kukucotsa pa phiri la Mulungu; ndipo ndinakuononga, kerubi wakuphimba iwe, kukucotsa pakati pa miyala yamoto.

17. Unadzikuza mtima cifukwa ca kukongola kwako, waipsa nzeru zako; cifukwa ca kuwala kwako ndakugwetsa pansi, ndakuika pamaso pa mafumu, kuti akupenye.

18. Mwa mphulupulu zako zocuruka ndi malonda ako osalungama waipsa malo ako opatulika; cifukwa cace ndaturutsa moto m'kati mwako wakunyeketsa iwe; ndipo ndakusandutsa mapulusa panthaka pamaso pa onse akuona.

19. Onse akudziwa iwe mwa mitundu ya anthu adzadabwa nawe; wasanduka coopsa, ndipo sudzakhalanso konse.

20. Anandidzeranso mau a Yehova, akuti,

21. Wobadwa ndi munthu iwe, lozetsa nkhope yako ku Zidoni, nuunenere;

22. uziti, Atero Ambuye Yehova, Taona, nditsutsana nawe Zidoni, ndipo ndidzalemekezedwa pakati pako; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova pakucita Ine maweruzo mwa uwu, ndi kuzindikiridwa Woyera mwa uwu.

23. Pakuti ndidzatumiza mliri ndi mwazi ilowe m'makwalala ace, ndi olasidwa adzagwa m'kati mwace ndi lupanga lougwera pozungulira ponse; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

24. Ndipo nyumba ya Israyeli siidzakhalanso nayo mitungwi yolasa, kapena minga yaululu ya ali yense wakuizinga ndi kuipeputsa; motero adzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 28