Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 24:12-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Nchito ya mphika ndi yolemetsa, koma dzimbiri lace lalikuru siliucokera, dzimbiri lace liyenera kumoto.

13. M'codetsa cako muli dama, popeza ndinakuyeretsa; koma sunayeretsedwa, sudzayeretsedwanso kukucotsera codetsa cako, mpaka nditakwaniritsa ukali wanga pa iwe.

14. Ine Yehova ndacinena, cidzacitika; ndipo ndidzacicita, sindidzamasula, kapena kulekerera, kapena kuwaleka, monga mwa njira zako, ndi monga umo unacitira adzakuweruza iwe, ati Ambuye Yehova.

15. Mau a Yehova anandidzeranso, akuti,

16. Wobadwa ndi munthu iwe, taona, ndikucotsera cokonda maso ako ndi cikomo, koma usamve cisoni, kapena kulira, kapena kudza misozi.

17. Usa moyo mosamveka, usalira wakufayo, dzimangire cilemba, nubvale nsapato ku mapazi ako, usaphimbe milomo yako, kapena kudya mkate wa anthu.

18. Ndipo nditalankhula ndi anthu m'mawa, madzulo ace mkazi wanga anamwalira; ndi m'mawa mwace ndinacita monga anandilamulira.

19. Nanena nane anthu, Simudzatiuza kodi zitani nafe izi muzicita?

20. Ndipo ndinanena nao, Anandidzera mau a Yehova, akuti,

21. Nena ndi nyumba ya Israyeli, Atero Ambuye Yehova, Taona, ndidzadetsa malo anga opatulika, ulemerero wa mphamvu yanu, cokonda m'maso mwanu, cimene moyo wanu ali naco cifundo; ndipo ana anu amuna ndi akazi otsalira inu adzagwa ndi lupanga.

22. Ndipo mudzacita monga umo ndacitira ine, osaphimba milomo yanu, kapena kudya mkate wa anthu.

23. Ndi zilemba zanu zidzakhala pamitu panu, ndi nsapato zanu ku mapazi anu, simudzacita cisoni kapena kulira, koma mudzaonda ndi mphulupulu zanu, ndi kubulirana wina ndi mnzace.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 24