Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 22:11-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Ndipo wina anacita conyansa ndi mkazi wa mnansi wace, winanso wadetsa mpongozi wace mwamanyazi, ndi wina mwa iwe anaipitsa mlongo wace mwana wamkazi wa atate wace.

12. Analandira mphotho mwa iwe kukhetsa mwazi, walandira phindu loonjezerapo, wanyengerera anansi ako ndi kuwazunza, ndipo wandiiwala Ine, ati Ambuye Yehova.

13. Taona, ndaomba manja pa phindu lako lonyenga waliona, ndi pa mwazi wokhala pakati pako.

14. Mtima wako udzaimika kodi, manja ako adzalimbikira masikuwo ndidzacita nawe? Ine Yehova ndanena, ndidzacicita.

15. Ndipo ndidzakumwaza mwa amitundu, ndi kukubalalitsa m'maiko, ndi kukuthera zodetsa zako zikucokere.

16. Ndipo udzaipsidwa mwa iwe wekha pamaso pa amitundu; motero udzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

17. Ndipo mau a Yehova anandidzera, akuti,

18. Wobadwa ndi munthu iwe, nyumba ya Israyeli yandikhalira mphala; onsewo ndiwo mkuwa, ndi seta, ndi citsulo, ndi ntobvu, m'kati mwa ng'anjo; ndiwo mphala zasiliva.

19. Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Popeza mwasanduka mphala nonsenu, cifukwa cace taonani, ndidzakusonkhanitsani m'kati mwa Yerusalemu.

20. Monga asonkhanitsamtapo wa siliva, ndi mkuwa, ndi citsulo, ndi ntobvu, ndi seta, m'kati mwa ng'anjo, kuzibvukutira moto, kuzisungunula momwemo, ndidzakusonkhanitsani mu mkwiyo wanga ndi ukali wanga, ndi kukuikani komweko, ndi kukusungunulani.

21. Inde ndidzakusonkhanitsani, ndi kukubvukutirani ndi moto wa kuzaza kwanga, ndipo mudzasungunuka pakati pace.

22. Monga siliva asungunuka m'kati mwa ng'anjo, momwemo inu mudzasungunuka m'kati mwace; motero mudzadziwa kuti Ine Yehova ndakutsanulirani ukali wanga.

23. Nandidzeranso mau a Yehova, akuti,

24. Wobadwa ndi munthu iwe, nena ndi Yuda, Iwe ndiwe dziko losayeretsedwa, losabvumbwa mvula tsiku la ukalilo.

25. Pali ciwembu ca aneneri ace pakati pace, ngati mkango wobangula womwetula nyama, analusira miyoyo, alanda cuma ndi za mtengo wace, acurukitsa amasiye pakati pace.

26. Ansembe ace acitira coipa cilamulo canga, nadetsa zopatulika zanga, sasiyanitsa pakati pa zopatulika ndi zosapatulika, ndipo sazindikiritsa anthu pakati pa zodetsa ndi zoyera, nabisira masabata anga maso ao; ndipo Ine ndidetsedwa pakati pao.

27. Akalonga ace m'kati mwace akunga afisi akumwetula nyama, kukhetsa mwazi, kuononga miyoyo, kuti aone phindu lonyenga.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 22