Monga siliva asungunuka m'kati mwa ng'anjo, momwemo inu mudzasungunuka m'kati mwace; motero mudzadziwa kuti Ine Yehova ndakutsanulirani ukali wanga.