Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 16:37-45 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

37. cifukwa cace taona, ndidzasonkhanitsa mabwenzi ako onse amene wakondwera nao, ndi onse unawakonda, pamodzi ndi onse unawada; inde ndidzawasonkhanitsira iwe pozungulira ponse, ndi kuwabvundukulira umarisece wako, kuti aone umarisece wako wonse.

38. Ndipo ndidzaweruza mlandu wako, monga aweruza akazi acigololo ndi okhetsa mwazi; ndipo ndidzakutengera mwazi wa ukali ndi wa nsanje.

39. Ndidzakuperekanso m'dzanja lao, ndipo adzagwetsa nyumba yako yacimphuli, ndi kugumula ziunda zako, nadzakubvula zobvala zako, ndi kulanda zokometsera zako zokongola, nadzakusiya wamarisece ndi wausiwa.

40. Ndipo adzamemezera iwe msonkhano, nadzakuponya miyala, ndi kukupyoza ndi malupanga ao.

41. Ndipo adzatentha nyumba zako ndi moto, nadzakuweruza pamaso pa akazi ambiri; ndipo ndidzakuleketsa kucita cigololo, ndipo sudzalipiranso mphotho yacigololo.

42. M'mwemo ukali wanga udzakhuta nawe, ndi nsanje yanga idzakucokera, ndipo ndidzakhala cete wosakwiyanso.

43. Popeza sunakumbukila masiku a ubwana wako, koma wandibvuta nazo zonsezi, cifukwa cace taona, Inenso ndidzakubwezera njira yako pamutu pako, ati Ambuye Yehova; ndipo sudzacita coipa ici coonjezerapo pa zonyansa zako zonse.

44. Taona, ali yense wonena miyambi adzakunenera mwambi uwu, wakuti, Monga mace momwemo mwana wace.

45. Iwe ndiwe mwana wa mako wonyansidwa naye mwamuna wace ndi ana ace, ndipo iwe ndiwe mng'ono wao wa akulu ako akunyansidwa ndi amuna ao ndi ana ao; mai wako ndiye Mhiti, ndi atate wako ndiye M-amori.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 16