Iwe ndiwe mwana wa mako wonyansidwa naye mwamuna wace ndi ana ace, ndipo iwe ndiwe mng'ono wao wa akulu ako akunyansidwa ndi amuna ao ndi ana ao; mai wako ndiye Mhiti, ndi atate wako ndiye M-amori.