Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 16:31-48 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

31. Pakumanga nyumba yako yacimphuli pa mphambano ziri zonse, ndi pomanga ciunda cako m'makwalala ali onse, sunakhala ngati mkazi wadama waphindu, popeza unapeputsa mphotho.

32. Ndiwe mkazi wokwatibwa wocita cigololo, wolandira alendo m'malo mwa mwamuna wace.

33. Anthu amaninkha akazi onse acigololo mphatso, koma iwe umaninkha mabwenzi ako onse mphatso zako ndi kuwalipira, kuti akudzere kucokera ku mbali zonse, kuti acite nawe cigololo.

34. M'mwemo usiyana konse ndi akazi ena m'cigololo cako; pakuti palibe wokutsata kucita nawe cigololo; popezanso uwalipira, koma sakupatsa iwe mphotho; potero usiyana nao konse ena.

35. Cifukwa cace, wacigololo iwe, tamvera mau a Yehova:

36. Atero Ambuye Yehova, Popeza ndalama zako zamwazika, nubvundukuka umarisece wako mwa cigololo cako ndi mabwenzi ako, ndi cifukwa ca mafano onse a zonyansa zako, ndi mwazi wa ana ako umene unawa patsa;

37. cifukwa cace taona, ndidzasonkhanitsa mabwenzi ako onse amene wakondwera nao, ndi onse unawakonda, pamodzi ndi onse unawada; inde ndidzawasonkhanitsira iwe pozungulira ponse, ndi kuwabvundukulira umarisece wako, kuti aone umarisece wako wonse.

38. Ndipo ndidzaweruza mlandu wako, monga aweruza akazi acigololo ndi okhetsa mwazi; ndipo ndidzakutengera mwazi wa ukali ndi wa nsanje.

39. Ndidzakuperekanso m'dzanja lao, ndipo adzagwetsa nyumba yako yacimphuli, ndi kugumula ziunda zako, nadzakubvula zobvala zako, ndi kulanda zokometsera zako zokongola, nadzakusiya wamarisece ndi wausiwa.

40. Ndipo adzamemezera iwe msonkhano, nadzakuponya miyala, ndi kukupyoza ndi malupanga ao.

41. Ndipo adzatentha nyumba zako ndi moto, nadzakuweruza pamaso pa akazi ambiri; ndipo ndidzakuleketsa kucita cigololo, ndipo sudzalipiranso mphotho yacigololo.

42. M'mwemo ukali wanga udzakhuta nawe, ndi nsanje yanga idzakucokera, ndipo ndidzakhala cete wosakwiyanso.

43. Popeza sunakumbukila masiku a ubwana wako, koma wandibvuta nazo zonsezi, cifukwa cace taona, Inenso ndidzakubwezera njira yako pamutu pako, ati Ambuye Yehova; ndipo sudzacita coipa ici coonjezerapo pa zonyansa zako zonse.

44. Taona, ali yense wonena miyambi adzakunenera mwambi uwu, wakuti, Monga mace momwemo mwana wace.

45. Iwe ndiwe mwana wa mako wonyansidwa naye mwamuna wace ndi ana ace, ndipo iwe ndiwe mng'ono wao wa akulu ako akunyansidwa ndi amuna ao ndi ana ao; mai wako ndiye Mhiti, ndi atate wako ndiye M-amori.

46. Ndi mkulu wako ndiye Samariya, wokhala ku dzanja lako lamanzere, iye ndi ana ace akazi; ndi mng'ono wako wokhala ku dzanja lako lamanja ndiye Sodomu ndi ana ace akazi.

47. Koma sunayenda m'njira zao, kapena kucita monga mwa zonyansa zao pang'ono pokha; unawaposa iwo m'kubvunda kwako, m'njira zako zonse.

48. Pali ine, ati Ambuye Yehova, Sodomu mng'ono wako sanacita, iye kapena ana ace akazi, monga umo unacitira iwe ndi ana ako akazi.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 16