Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 13:2-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Wobadwa ndi munthu iwe, Unenere za aneneri a Israyeli onenerawo, nuziti nao onenera za m'mtima mwao mwao, Tamverani mau a Yehova.

3. Atero Ambuye Yehova, Tsoka aneneri opusawo akutsata mzimu wao wao, cinkana sanaona kanthu.

4. Aneneri ako, Israyeli, akhala ngati nkhandwe m'mapululu.

5. Simunakwera kuima mopasuka, kapena kumanganso linga la nyumba ya Israyeli, kuima kunkhondo tsiku la Yehova.

6. Iwo aona zopanda pace, ndi phenda labodza amene anena, Atero Yehova; koma Yehova sanawatuma, nayembekezetsa anthu kuti mauwo adzakhazikika.

7. Simunaona masomphenya opanda pace kodi? simunanena ula wabodza kodi? pakunena inu, Atero Yehova; cinkana sindinanena?

8. Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Popeza mwanena zopanda pace, ndi kuona mabodza, cifukwa cace taonani, ndikhala Ine wotsutsana nanu, ati Ambuye Yehova.

9. Ndi dzanja langa lidzakhala lotsutsana nao aneneri akuona zopanda pace, ndi kupenda za bodza; sadzakhala mu msonkhano wa anthu anga, kapena kulembedwa m'buku lolembedwamo nyumba ya Israyeli, kapena kulowa m'dziko la Israyeli; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova,

10. Popeza, inde popeza asokeretsa anthu anga, ndi kuti, Mtendere, pokhala palibe mtendere; ndipo anthu akamanga linga, aneneriwo alimata ndi dothi losapondeka;

11. uziti nao olimata ndi dothi losapondeka, kuti lidzagwa, lidzabvumbidwa ndi mvula yaikuru; ndi inu, matalala akuru, mudzagwa; ndi mkuntho udzalithithimula.

12. Ndipo taonani, litagwa linga, sadzanena nanu kodi, Liri kuti dothi munalimata nalo?

13. Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Ndidzalithithimula ndi mkuntho m'ukali wanga; ndipo lidzabvumbidwa ndi mvula yaikuru mu mkwiyo wanga, ndi matalala akuru adzalitha m'ukali wanga.

14. M'mwemo ndidzagumula linga munalimata ndi dothi losapondeka, ndi kuligwetsa pansi; kuti maziko ace agadabuke, ndipo lidzagwa; ndi inu mudzathedwa pakati pace; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 13