Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Ndidzalithithimula ndi mkuntho m'ukali wanga; ndipo lidzabvumbidwa ndi mvula yaikuru mu mkwiyo wanga, ndi matalala akuru adzalitha m'ukali wanga.