Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 13:13-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Ndidzalithithimula ndi mkuntho m'ukali wanga; ndipo lidzabvumbidwa ndi mvula yaikuru mu mkwiyo wanga, ndi matalala akuru adzalitha m'ukali wanga.

14. M'mwemo ndidzagumula linga munalimata ndi dothi losapondeka, ndi kuligwetsa pansi; kuti maziko ace agadabuke, ndipo lidzagwa; ndi inu mudzathedwa pakati pace; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

15. M'mwemo ndidzakwaniritsa ukali wanga pa lingalo, ndi pa iwo analimata ndi dothi losapondeka, ndipo ndidzati kwa inu, Lingalo palibe, ndi olimata palibe,

16. ndiwo aneneri a Israyeli akunenera za Yerusalemu, nauonera masomphenya a mtendere, pamene palibe mtendere, ati Ambuye Yehova.

17. Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, uziika nkhope yako itsutsane nao ana akazi a anthu ako, akunenera za m'mtima mwao, nunenere cowatsutsa,

18. nuziti, Atero Ambuye Yehova, Tsoka akazi osoka zophimbira mfundo zonse za dzanja, ndi iwo okonza zokuta mitu za misinkhu iri yonse, kuti asake miyoyo! Kodi musaka miyoyo ya anthu anga ndi kudzisungira miyoyo yanu?

19. Ndipo mundidetsa mwa anthu anga kulandirapo barele wodzala manja, ndi zidutsu za mkate, kuipha miyoyo yosayenera kufa, ndi kusunga miyoyo yosayenera kukhala ndi moyo, ndi kunena mabodza kwa anthu anga omvera bodza.

20. Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Taonani, nditsutsana nazo zophimbira zanu, zimene musaka nazo miyoyo komweko, kululuza; ndipo ndidzazikwatula m'manja mwanu, ndi kuimasula, ndiyo miyoyo muisaka kululuza.

21. Zokuta mitu zanu zomwe ndidzazing'amba, ndi kulanditsa anthu anga m'manja mwanu; ndipo sadzakhalanso m'mphamvu mwanu kusakidwa; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

22. Popeza mwamvetsa cisoni ndi mabodza mtima wa wolungama, amene sindinamvetsa cisoni Ine, ndi kumlimbitsa manja woipa, kuti asabwerere kuleka njira yace yoipa, ndi kusungidwa wamoyo;

23. cifukwa cace simudzaonanso zopanda pace, kapena kupenda; koma ndidzalanditsa anthu anga m'manja mwanu; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 13