Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 12:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Mau a Yehova anandidzeranso, ndi kuti,

2. Wobadwa ndi munthu iwe, ukhala pakati pa nyumba yampanduko, yokhala nao maso akuonera, koma osaona; ndi makutu akumvera, koma osamva; pakuti iwo ndiwo nyumba yampanduko.

3. Potero wobadwa ndi munthu iwe, udzikonzeretu akatundu a pa ulendo wa kundende, nucoke usana pamaso pao, ucoke pakhala iwepo kumka malo ena pamaso pao; kapena adzacizindikira, angakhalendiwo nyumbayopanduka.

4. Uziturutsa akatundu ako usana pamaso pao, ngati a pa ulendo wa kundende; ndipo madzulo uzituruka wekha pamaso pao, monga amaturuka olowa kundende.

5. Udziboolere khoma pamaso pao, nuwaturutsire akatundu pamenepo,

6. Pamaso pao uwasenze paphewa pako, ndi kuwaturutsa kuli mdima, nuphimbe nkhope yako kuti usapenye dziko; popeza ndakuika cizindikilo ca nyumba ya Israyeli.

7. Ndipo ndinacita monga momwe anandilamulira, ndinaturutsa akatundu anga usana, ngati a pa ulendo wa kundende, ndi madzulo ndinaboola pakhoma ndi dzanja langa, ndinawaturutsa pali mdima, ndi kuwasenza paphewa panga pamaso: pao.

8. Ndipo m'mawa mau a Yehova anandidzera, ndi kuti,

9. Wobadwa ndi munthu iwe, kodi nyumba ya Israyeli, nyumba yampanduko, siinati kwa iwe. Ucitanji?

10. Unene nao, Atero Ambuye Yehova, Katundu uyu anena za kalonga wa m'Yerusalemu, ndi nyumba yonse ya Israyeli yokhala pakati pao.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 12