Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 11:9-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Ndipo ndidzakuturutsani m'kati mwace, ndi kukuperekani m'manja a alendo, ndi kucita maweruzo pakati panu.

10. Mudzagwa ndi lupanga, ndidzakuweruzirani ku malire a Israyeli; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

11. Mudzi uno sudzakhala mphika wanu, ndi inu simudzakhala nyama m'kati mwace, ndidzakuweruzirani ku malire a Israyeli;

12. ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pakuti simunayenda m'malemba anga, kapena kucita maweruzo anga, koma mwacita monga mwa maweruzo a amitundu okhala pozungulira panu.

13. Ndipo kunali, pakunenera ine, anamwalira Pelatiya mwana wa Benaya. Pamenepo ndinagwa nkhope yanga pansi, ndi kupfuula ndi mau akuru, ndi kuti, Kalanga ine, Yehova Mulungu! mudzatsiriza kodi otsala a Israyeli?

14. Ndipo mau a Yehova anandidzera kuti,

15. Wobadwa ndi munthu iwe, abale ako, inde abale ako amuna a cibale cako, ndi nyumba yonse ya Israyeli, yonseyi ndiwo amene okhala m'Yerusalemu ananena nao, Muzikhala kutali kwa Yehova; dziko ili lapatsidwa kwa ife, likhale colowa cathu;

16. cifukwa cace uziti, Atero Yehova Mulungu, Ngakhale ndawacotsa kutali mwa amitundu, ngakhalenso ndawabalalikitsa m'maiko, koma ndidzawakhalira malo opatulika kanthawi ku maiko adafikako.

17. Cifukwa cace uziti, Atero Yehova Mulungu, Ndidzakumemezani ku mitundu ya anthu, ndi kukusonkhanitsani mucoke m'maiko m'mene munabalalikiramo, ndipo ndidzakuninkhani dziko la Israyeli.

18. Ndipo adzafikako, nadzacotsako zonyansa zace zonse, ndi zace zonse zakuipitsamo.

19. Ndipo ndidzawapatsa mtima umodzi, ndi kuika mzimu watsopano m'kati mwao; ndipo ndidzawacotsera mtima wamwala m'thupi mwao, ndi kuwapatsa mtima wamnofu;

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 11