Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezekieli 1:20-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Kuli konse mzimu ukuti umuke, zinamuka komwe mzimu ukuti umuke; ndi njingazi zinanyamuka pambali pa izo; pakuti mzimu wa zamoyozo unali m'njingazo.

21. Poyenda zija zinayenda izi, poima zija zinaima izi; ndipo ponyamuka pansi zija njingazi zinanyamuka pambali pa izo; pakuti mzimu wa zamoyozo unali mu njingazi.

22. Ndi pa mitu ya zamoyozi panali cifaniziro ca thambo, monga mawalidwe a krustalo woopsa, loyalika pamwamba pamitu pao.

23. Ndi pansi pa thambolo mapiko ao analunjikana, lina kulunjika ku linzace; ciri conse cinali nao mapiko awiri akuphimba matupi ao, cakuno ndi cauko.

24. Ndipo pakuyenda izi ndinamva mkokomo wa mapiko ao, ngati mkokomo wa madzi akulu, ngati mau a Wamphamvuyonse, phokoso lakusokosera ngati phokoso la ankhondo; pakuima zinagwetsa mapiko ao.

25. Ndipo panamveka mau pamwamba pa thambolo linali pamwamba pa mitu yao; pakuima izi zinagwetsa mapiko ao.

26. Ndi pamwamba pa thambo linali pamitu pao panali cifaniziro ca mpando wacifumu, maonekedwe ace ngati mwala wa safiro; ndipo pa cifaniziro ca mpando wacifumu panali cifaniziro ngati maonekedwe ace a munthu wokhala pamwamba pace.

27. Ndipo ndinapenya ngati citsulo cakupsa, ngati maonekedwe ace a moto m'kati mwace pozungulira pace, kuyambira maonekedwe a m'cuuno mwace ndi kumwamba kwace; ndipo kuyambira maonekedwe a m'cuuno mwace ndi kunsi kwace ndinaona ngati maonekedwe ace a moto; ndi kunyezimira kudamzinga.

28. Ngati maonekedwe a utawaleza uli m'mtambo tsiku la mvula, momwemo maonekedwe a kunyezimira kwace pozungulira pace. Ndiwo maonekedwe a cifaniziro ca ulemerero wa Yehova. Ndipo pakucipenya ndinagwa nkhope pansi, ndipo ndinamva mau a wina wakunena.

Werengani mutu wathunthu Ezekieli 1