Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezara 7:13-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Ndilamulira kuti onse a ana a Israyeli, ndi ansembe ao, ndi Alevi, m'ufumu wanga, ofuna eni ace kumuka ku Yerusalemu, apite nawe.

14. Popeza utumidwa wocokera pamaso pa mfumu ndi aphungu ace asanu ndi awiri, kufunsira za Yuda ndi Yerusalemu monga mwa lamulo la Mulungu wako liri m'dzanja lako,

15. ndi kumuka nazo siliva ndi golidi, zimene mfumu ndi aphungu ace, anapereka mwaufulu kwa Mulungu wa Israyeli, mokhala mwace muli m'Yerusalemu,

16. pamodzi ndi siliva ndi golidi ziri zonse ukazipeza m'dziko lonse la ku Babulo, pamodzi ndi copereka caufulu ca anthu, ndi ca ansembe, akuperekera mwaufulu nyumba ya Mulungu wao iri ku Yerusalemu;

17. m'mwemo uzifulumira kugula ndi ndalama iyi ng'ombe, nkhosa zamphongo, ana a nkhosa, pamodzi ndi nsembe zao zaufa, ndi nsembe zao zothira; ndi kuzipereka pa guwa la nsembe la nyumba ya Mulungu wanu yokhala ku Yerusalemu.

18. Ndipo ciri conse cidzakomera iwe ndi abale ako kucita nazo siliva ndi golidi zotsala, ici mucite monga mwa cifuniro ca Mulungu wanu.

19. Ndipo zipangizozo akupatsa za utumiki wa nyumba ya Mulungu wako, uzipereka pamaso pa Mulungu wa ku Yerusalemu.

20. Ndi zina zotsala zakusowa nyumba ya Mulungu wako, zikayenera uzipereke, uzipereke zocokera ku nyumba ya cuma ca mfumu.

21. Ndipo ine Aritasasta, mfumu ine, ndilamulira osunga cuma onse okhala tsidya lija la mtsinjewo, kuti ciri conse akupemphani Ezara wansembe, mlembi wa lamulo la Mulungu wa Kumwamba, cicitike mofulumira;

Werengani mutu wathunthu Ezara 7