Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezara 7:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Zitatha izi tsono, pokhala mfumu Aritasasta mfumu ya Perisiya, anadza Ezara mwana wa Seraya, mwana wa Azariya, mwana wa Hilikiya,

2. mwana wa Salumu, mwana wa Zadoki, mwana wa Ahitubu,

3. mwana wa Amariya, mwana wa Azariya, mwana wa Meraioti,

4. mwana wa Zerahiya, mwana wa Uzi, mwana wa Buki,

5. mwana wa Abisuwa mwana wa Pinehasi, mwana wa Eleazara, mwana wa Aroni wansembe wamkuru.

6. Ezara amene anakwera kucokera ku Babulo, ndiye mlembi waluntha m'cilamulo ca Mose, cimene Yehova Mulungu wa Israyeli adacipereka; ndipo mfumu inampatsa copempha iye conse, monga linamkhalira dzanja la Yehova Mulungu wace.

7. Nakweranso kumka ku Yerusalemu ena a ana a Israyeli, ndi ansembe, ndi Alevi, ndi oyimbira, ndi odikira, ndi Anetini, caka cacisanu ndi ciwiri ca Aritasasta mfumu.

8. Ndipo iye anafika ku Yerusalemu mwezi wacisanu, ndico caka cacisanu ndi ciwiri ca mfumu.

9. Pakuti tsiku loyamba la mwezi woyamba, ndilo ciyambi ca ulendo wokwera kucokera ku Babulo, ndi tsiku lacimodzi la mwezi wacisanu anafika ku Yerusalemu, monga linamkhalira dzanja lokoma la Mulungu wace.

10. Pakuti Ezara adaikiratu mtima wace kucifuna cilamulo ca Yehova, ndi kucicita, ndi kuphunzitsa m'Israyeli malemba ndi maweruzo.

Werengani mutu wathunthu Ezara 7