Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezara 6:11-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Ndalamuliranso kuti ali yense adzasintha mau awa, usololedwe mtanda kunyumba kwace, namkweze, nampacike pomwepo; niyesedwe dzala nyumba yace cifukwa ca ici;

12. ndipo Mulungu wokhalitsa dzina lace komweko agwetse mafwnu onse ndi mitundu yonse ya anthu, akuturutsa dzanja lao kusintha mau awa, kuononga nyumba ya Mulungu iri ku Yerusalemu. Ine Dariyo ndalamulira, cicitike msanga.

13. Pamenepo Tatinai kazembe wa tsidya lino la mtsinjewo, Setara Bozenai, ndi anzao, popeza mfumu Dariyo adatumiza mau, anacita momwemo cofulumira.

14. Ndipo akulu a Ayuda anamanga opanda cosoweka, mwa kunenera kwa mneneri Hagai, ndi Zekariya mwana wa Ido. Naimanga, naitsiriza, monga mwa lamulo la Mulungu wa Israyeli, ndi monga mwa lamulo la Koresi, ndi Dariyo, ndi Aritasasta mfumu ya Perisiya,

15. Nitsirizidwa nyumba iyi tsiku lacitatu la mwezi wa Adara, ndico caka cacisanu ndi cimodzi ca ufumu wa Dariyo mfumu.

16. Ndipo ana a Israyeli, ansembe ndi Alevi, ndi ana otsala a ndende, anapereka nyumba iyi ya Mulungu mokondwera.

17. Ndipo popatulira nyumba iyi ya Mulungu anapereka ng'ombe zana limodzi, nkhosa zamphongo mazana awiri, ana a nkhosa mazana anai, ndi za nsembe yazolakwa ya Aisrayeli onse atonde khumi ndi awiri, monga mwa kuwerenga kwace kwa mapfuko a Israyeli.

18. Naika ansembe m'magawo mwao, ndi Alevi m'magawidwe mwao, atumikire Mulungu wokhala ku Yerusalemu, monga mulembedwa m'buku la Mose.

19. Ndipo ana a ndende anacita Paskha tsiku lakhumi ndi cinai la mwezi woyamba.

20. Pakuti ansembe ndi Alevi anadziyeretsa pamodzi, anayera onsewo, naphera Paskha cifukwa ca ana onse a ndende, ndi abale ao ansembe, ndi iwo okha.

21. Ndipo ana a Israyeli obwera kundende, ndi yense wakudzipatulira kucokera conyansa ca amitundu, kutsata iwowa, kufuna Yehova Mulungu wa Israyeli, anadza,

22. nasunga madyerero a mkate wopanda cotupitsa masiku asanu ndi awiri ndi cimwemwe; pakuti Yehova adawakondweretsa, nawatembenuzira mtima wa mfumu ya Asuri, kulimbitsa manja ao mu nchito ya nyumba ya Mulungu, Mulungu wa Israyeli.

Werengani mutu wathunthu Ezara 6