Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezara 4:1-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Atamva tsono a adani Yuda ndi Benjamini kuti ana aja a ndende analikumangira Yehova Mulungu wa Israyeli Kacisi,

2. anayandikira kwa Zerubabele, ndi kwa akulu a nyumba za makolo, nanena nao, Timange pamodzi nanu; pakuti timfuna Mulungu wanu monga inu, ndipo timamphera nsembe ciyambire masiku a Ezaradoni mfumu ya Asuri, amene anatikweretsa kuno.

3. Koma Zerubabele, ndi Yesuwa, ndi akuru otsala a nyumba za makolo a Israyeli, anati kwa iwo, Sikuyenera ndi inu ndi ife kumangira Mulungu wathu nyumba, koma ife tokha pamodzi tidzamangira Yehova Mulungu wa Israyeli, monga mfumu Koresi mfumu ya Perisiya watilamulira.

4. Pamenepo anthu a m'dziko anafoketsa manja a anthu Ayuda, nawabvuta pomanga,

5. nalembera opangira atsutsane nao, nafafanize uphungu wao, masiku onse a Koresi mfumu ya Perisiya, mpaka ufumu wa Dariyo mfumu ya Perisiya.

6. Ndipo pokhala mfumu Ahaswero, poyambira ufumu wace, analembera cowaneneza okhala m'Yuda ndi m'Yerusalemu.

7. Ndipo masiku a Aritasasta Bisilamu, Mitiredati, Tabeeli, ndi anzao otsala, analembera kwa Aritasasta mfumu ya Perisiya; ndi cilembedwe cace ca kalatayo anamlemba m'Ciaramu, namsanduliza m'Ciaramu.

8. Rehumu ciwinda ca malamulo, ndi Simsai mlembi, analemba kalata kwa mfumu Aritasasta, wakutsutsana naye Yerusalemu motere:

9. nalembera Rehumu ciwinda ca malamulo, ndi Simsai mlembi, ndi anzace otsala; Adinai, ndi Afarisatikai, Ataripilai, Afarisai, Arekavai, Ababulo, Asusanekai, Adehai, Aelimai,

10. ndi amitundu otsala amene, Osinapera wamkuru ndi womveka adawatenga mikoli, nawakhalitsa m'mudzi wa Samariya, ndi m'dziko lotsala tsidya lino la mtsinje wa Firate, pa nthawi yakuti.

11. Zolembedwa m'kalatayo anamtumiza kwa Aritasasta mfumu ndizo: Akapolo anu, anthu a tsidya lino la mtsinjewo, ndi pa nthawi yakuti.

Werengani mutu wathunthu Ezara 4