Adziwe mfumu kuti, Ayuda adakwerawo ocokera kwanu atifikira ife ku Yerusalemu, alikumanga mudzi uja wopanduka ndi woipa, alikutsiriza malinga ace, nalumikiza maziko ace.