Koma Zerubabele, ndi Yesuwa, ndi akuru otsala a nyumba za makolo a Israyeli, anati kwa iwo, Sikuyenera ndi inu ndi ife kumangira Mulungu wathu nyumba, koma ife tokha pamodzi tidzamangira Yehova Mulungu wa Israyeli, monga mfumu Koresi mfumu ya Perisiya watilamulira.