Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Estere 9:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Mwezi wakhumi ndi ciwiri tsono, ndiwo mwezi wa Adara, tsiku lace lakhumi ndi citatu, mau a mfumu ndi lamulo lace ali pafupi kucitika, tsikuli adani a Ayuda anayesa kuwacitira ufumu, koma cinasinthika; popeza Ayuda anacitira ufumu iwo odana nao;

2. pakuti Ayuda anasonkhana pamodzi m'midzi mwao, m'maiko onse a mfumu Ahaswero, kuwathira manja ofuna kuwacitira coipa, ndipo palibe munthu analimbika pamaso pao; popeza kuopsa kwao kudawagwera mitundu yonse ya anthu.

3. Ndipo akalonga onse a maikowo, ndi akazembe, ndi ziwanga, ndi iwo ocita nchito ya mfumu, anathandiza Ayuda; popeza kuopsa kwa Moredekai kudawagwera.

4. Pakuti Moredekai anali wamkuru m'nyumba ya mfumu, ndi mbiri yace idabuka m'maiko onse; pa kuti munthuyu Moredekai anakula-kulabe.

5. Ndipo Ayuda anakantha adani ao onse, kuwakantha ndi lupanga, ndi kuwapulula, nacitira odana nao monga anafuna.

Werengani mutu wathunthu Estere 9