Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Estere 8:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Tsiku lomwelo mfumu Ahaswero anampatsa mkazi wamkuru Estere nyumba ya Hamani mdani wa Ayuda, Nafika Moredekai pamaso pa mfumu; pakuti Estere adamuuza za cibale cace.

2. Ndipo mfumu inabvula mphete yace adailanda kwa Hamani, naipereka kwa Moredekai. Ndi Estere anaika Moredekai akhale woyang'anira nyumba ya Hamani.

3. Nanenanso Estere pamaso pa mfumu, nagwa ku mapazi ace, nalira misozi, nampembedza kuti acotse coipaco ca Hamani wa ku Agagi, ndi ciwembu adacipangira Ayuda,

4. Ndipo mfumu inaloza Estere ndi ndodo yacifumu yagolidi. Nanyamuka Estere, naima pamaso pa mfumu.

5. Nati, Cikakomera mfumu, ndipo ngati yandikomera mtima, niciyenera kwa mfumu, ngatinso ndimcititsa kaso, alembere cosintha mau a akalata a ciwembu ca Hamani mwana wa Hamedata wa ku Agagi, amene adawalembera kuononga Ayuda okhala m'maiko onse a mfumu;

6. pakuti ndidzapirira bwanji pakuciona coipa cirikudzera amtundu wanga, kapena ndidzapirira bwanji pakuciona cionongeko ca pfuko langa?

7. Pamenepo mfumu Ahaswero anati kwa mkazi wamkuru Estere, ndi kwa Moredekai Myuda, Taonani, ndampatsa Estere nyumba ya Hamani, ndi iyeyu anampacika pamtanda, cifukwa anaturutsa dzanja lace pa Avuda,

8. Mulembere inunso kwa Ayuda monga mufuna, m'dzina la mfumu, nimusindikize ndi mphete ya mfumu; pakuti kalata wolembedwa m'dzina la mfumu, ndi kusindikizika ndi mphete ya mfumu, palibe munthu akhoza kumsintha.

Werengani mutu wathunthu Estere 8