Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Estere 6:10-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Pamenepo mfumu inati kwa Hamani, Fulumira, tenga cobvala ndi kavalo monga umo wanenera, nucitire cotero Moredakai Myudayo, wokhala pa cipata ca mfumu; kasasowepo kanthu ka zonse wazinena.

11. Ndipo Hamani anatenga cobvala ndi kavalo, nabveka Moredekai, namuyendetsa pa kavalo m'khwalala la m'mudzi, napfuula pamaso pace, Azitero naye munthu amene mfumu ikondwera kumcitira ulemu.

12. Ndipo Moredekai anabweranso ku cipata ca mfumu. Koma Hamani anafulumira kumka kwao, wacisoni ndi wopfunda mutu wace.

13. Ndipo Hamani anafotokozera Zeresi mkazi wace, ndi mabwenzi ace onse, zonse zidamgwera, Nanena naye anzeru ace, ndi Zeresi mkazi wace, Moredekai amene wayamba kutsika pamaso pace, akakhala wa mbumba ya Ayuda, sudzamlaka; koma udzagwada pamaso pace.

14. Akali cilankhulire naye, anafika adindo a mfumu, nafulumira kumtenga Hamani kumka naye kumadyerero adawakonzera Estere.

Werengani mutu wathunthu Estere 6