Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Estere 1:8-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Ndi mamwedwewo anali monga mwa lamulo; panalibe kukakamiza; pakuti mfumu idaikira akulu onse a nyumba yace motero, kuti acite monga momwe akhumba ali yense.

9. Vasiti yemwe, mkazi wamkuru, anakonzera akazi madyerero m'nyumba yacifumu ya mfumu Ahaswero.

10. Tsiku lacisanu ndi ciwiri, pokondwera mtima wa mfumu ndi vinyo, iye anauza Mehumani, Bizita, Haribona, Bigita, ndi Abagita, Zetara, ndi Karikasi, adindo asanu ndi awiriwo akutumikira pamaso pa mfumu Ahaswero,

11. abwere naye Vasiti mkazi wamkuru pamaso pa mfumu ndi korona wacifumu, kuonetsa anthu ndi akuru kukoma kwace; popeza anali wokongola maonekedwe ace.

12. Koma Vasiti mkazi wamkuruyo anakana kudza pa mau a mfumu adamuuza adindowo; potero mfumu idapsa mtima ndithu, ndi mkwiyo wace unatentha m'kati mwace.

13. Pamenepo mfumu inanena kwa eni nzeru, akudziwa za m'tsogolo, mfumu idafotero nao onse akudziwa malamulo ndi maweruzo,

14. a pafupi naye ndiwo Karisena. Setara, Adimata, Tarisisi, Meresi, Marisena, ndi Memukana, akalonga asanu ndi awiri a Perisiya ndi Mediya, openya nkhope ya mfumu ndi kukhala oyamba m'ufumu.

15. Anati, Tidzacitanji naye mkazi wamkuru Vasiti monga mwa malamulo, popeza sanacita comuuza mfumu Ahaswero mwa adindo?

16. Ndi Memukana anati pamaso pa mfumu ndi akalonga, Vasiti mkazi wamkuru sanalakwira mfumu yekha, komanso akalonga onse, ndi mitundu yonse ya anthu okhala m'maiko onse a mfumu Ahaswero.

17. Pakuti macitidwe awa a mkazi wamkuruyo adzabuka kufikira akazi onse, kupeputsa amuna ao pamaso pao; anthu akati, Mfumu Ahaswero anati abwere naye Vasiti mkazi wamkuru pamaso pace, koma sanadza iye.

18. Inde tsiku lomwelo akazi akuru a Perisiya ndi Mediya, atamva macitidwe a mkazi wamkuruyo, adzatero nao momwemo kwa akalonga onse a mfumu. Ndi cipeputso ndi mkwiyo zidzacuruka.

19. Cikakomera mfumu, aturuke mau acifumu pakamwa pace, nalembedwe m'malamulo a Aperisiya ndi Amediya, angasinthike, kuti Vasiti asalowenso pamaso pa mfumu Ahaswero; ndi mfumu aninkhe cifumu cace kwa mnzace womposa iye.

20. Ndipo mau amene adzaika mfumu akamveka m'ufumu wace wonse, (pakuti ndiwo waukuru), akazi onse adzacitira amuna ao ulemu, akulu ndi ang'ono.

21. Ndipo mauwo anakonda mfumu ndi akalonga; ndi mfumu inacita monga mwa mau a Memukana,

22. natumiza akalata ku maiko onse a mfumu, ku dziko liri lonse monga mwa cilembedwe cao, ndi ku mtundu uli wonse monga mwa cinenedwe cao, kuti mwamuna ali yense akhale wamkuru m'nyumba yace yace, nawabukitse monga mwa cinenedwe ca anthu amtundu wace.

Werengani mutu wathunthu Estere 1