Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Estere 1:5-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Atatha masikuwa, mfumu inakonzera madyerero anthu onse okhala m'cinyumba ca ku Susani, akulu ndi ang'ono, masiku asanu ndi awiri, ku bwalo la munda wa maluwa wa ku cinyumba ca mfumu;

6. panali nsaru zolenjeka zoyera, zabiriwiri, ndi zamadzi, zomangika ndi zingwe za thonje labafuta, ndi lofiirira, pa zigwinjiri zasiliva, ndi nsanamira zansangalabwi; makama anali a golidi ndi siliva pa mayalidwe a miyala yofiira, ndi yoyera, ndi yoyezuka, ndi yakuda.

7. Nawapatsa cakumwa m'zomwera zagolidi, zomwerazo nzosiyana-siyana, ndi vinyo wacifumu anacuruka, monga mwa ufulu wa mfumu.

8. Ndi mamwedwewo anali monga mwa lamulo; panalibe kukakamiza; pakuti mfumu idaikira akulu onse a nyumba yace motero, kuti acite monga momwe akhumba ali yense.

9. Vasiti yemwe, mkazi wamkuru, anakonzera akazi madyerero m'nyumba yacifumu ya mfumu Ahaswero.

10. Tsiku lacisanu ndi ciwiri, pokondwera mtima wa mfumu ndi vinyo, iye anauza Mehumani, Bizita, Haribona, Bigita, ndi Abagita, Zetara, ndi Karikasi, adindo asanu ndi awiriwo akutumikira pamaso pa mfumu Ahaswero,

11. abwere naye Vasiti mkazi wamkuru pamaso pa mfumu ndi korona wacifumu, kuonetsa anthu ndi akuru kukoma kwace; popeza anali wokongola maonekedwe ace.

12. Koma Vasiti mkazi wamkuruyo anakana kudza pa mau a mfumu adamuuza adindowo; potero mfumu idapsa mtima ndithu, ndi mkwiyo wace unatentha m'kati mwace.

13. Pamenepo mfumu inanena kwa eni nzeru, akudziwa za m'tsogolo, mfumu idafotero nao onse akudziwa malamulo ndi maweruzo,

14. a pafupi naye ndiwo Karisena. Setara, Adimata, Tarisisi, Meresi, Marisena, ndi Memukana, akalonga asanu ndi awiri a Perisiya ndi Mediya, openya nkhope ya mfumu ndi kukhala oyamba m'ufumu.

15. Anati, Tidzacitanji naye mkazi wamkuru Vasiti monga mwa malamulo, popeza sanacita comuuza mfumu Ahaswero mwa adindo?

16. Ndi Memukana anati pamaso pa mfumu ndi akalonga, Vasiti mkazi wamkuru sanalakwira mfumu yekha, komanso akalonga onse, ndi mitundu yonse ya anthu okhala m'maiko onse a mfumu Ahaswero.

Werengani mutu wathunthu Estere 1