Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Estere 1:2-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Masiku ajawo, pokhala Ahaswero pa mpando wa ufumu wace uli m'cinyumba ca ku Susani,

3. caka cacitatu ca ufumu wace, anakonzera madyerero akalonga ace onse, ndi omtumikira; amphamvu a Perisiya ndi Mediya, omveka ndi akalonga a maikowo anakhala pamaso pace,

4. pamene anaonetsa zolemera za ufumu wace waulemu, ndi ulemerero wa ukulu wace woposa, masiku ambiri, ndiwo masiku zana limodzi, mphambu makumi asanu ndi atatu.

5. Atatha masikuwa, mfumu inakonzera madyerero anthu onse okhala m'cinyumba ca ku Susani, akulu ndi ang'ono, masiku asanu ndi awiri, ku bwalo la munda wa maluwa wa ku cinyumba ca mfumu;

6. panali nsaru zolenjeka zoyera, zabiriwiri, ndi zamadzi, zomangika ndi zingwe za thonje labafuta, ndi lofiirira, pa zigwinjiri zasiliva, ndi nsanamira zansangalabwi; makama anali a golidi ndi siliva pa mayalidwe a miyala yofiira, ndi yoyera, ndi yoyezuka, ndi yakuda.

7. Nawapatsa cakumwa m'zomwera zagolidi, zomwerazo nzosiyana-siyana, ndi vinyo wacifumu anacuruka, monga mwa ufulu wa mfumu.

Werengani mutu wathunthu Estere 1