Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 8:8-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Pamenepo Farao anaitana Mose ndi Aroni, nati, Mundipembere Yehova, kuti andicotsere ine ndi anthu anga aculewo; ndipo ndidzalola anthu amuke, kuti amphere Yehova nsembe.

9. Koma Mose anati kwa Farao, Ulemu ndi wanu, wa ine ai; ndipembere inu ndi anyamata anu ndi anthu anu liti, kuti aonongeke aculewo, acokere inu ndi nyumba zanu, atsale m'nyanja mokha?

10. Ndipo anati, Mawa. Nati Mose, Kukhale monga mau anu, kuti mudziwe, kuti palibe wina wonga Yehova Mulungu wathu.

11. Ndipo acule adzacokera inu, ndi nyumba zanu, ndi anyamata anu, ndi anthu anu; adzatsala m'nyanja mokha.

12. Ndipo Mose ndi Aroni anaturuka kwa Farao; ndi Mose anapfuulira kwa Yehova kunena za acule amene adawaika pa Farao.

13. Ndipo Yehova anacita monga mwa mau a Mose; nafa aculewo kucokera m'zinyumba, ndi m'mabwalo, ndi m'minda.

14. Ndipo anawaola miulu-miulu; ndi dziko linanunkha.

15. Koma pamene Farao, anaona kuti panali kupuma, anaumitsa mtima wace, osamvera iwo; monga adalankhula Yehova.

16. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni, Samula ndodo yako, nupande pfumbi lapansi, kuti lisanduke nsabwe m'dziko lonse la Aigupto.

17. Ndipo anacita comweco; pakuti Aroni anasamula dzanja lace ndi ndodo yace, napanda pfumbi lapansi, ndipo panali nsabwe pa anthu ndi pa zoweta; pfumbi lonse lapansi liinasanduka nsabwe m'dziko lonse la Aigupto.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 8