Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 7:14-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Walemera mtima wa Farao, akana kulola anthu apite,

15. Muka kwa Farao m'mawa; taona, aturuka kumka kumadzi; nuime kumlinda m'mbali mwa nyanja; ndi ndodo idasanduka njokayo uigwire m'dzanja lako.

16. Ndipo ukanena naye, Yehova, Mulungu wa Ahebri anandituma kwa inu, ndi kuti, Lola anthu anga amuke kuti anditumukire m'cipululu; koma, taona, sunamvera ndi pano.

17. Atero Yehova, Ndi ici udzadziwa kuti Ine ndine Yehova: taonani, ndidzapanda madzi ali m'nyanja ndi ndodo iri m'dzanja langa, ndipo adzasanduka mwazi.

18. Ndi nsomba ziri m'nyanja zidzafa, ndi nyanja idzanunkha; ndi Aaigupto adzacita mtima useru ndi kumwa madzi a m'nyanjamo.

19. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni, Tenga ndodo yako, nutambasule dzanja lako pa madzi a m'Aigupto, pa nyanja yao, pa ngalande zao, ndi pa matamanda ao, ndi pa matawale ao onse amadzi, kuti asanduke mwazi; mukhale mwazi m'dziko lonse la Aigupto, m'zotengera zamtengo, ndi zamwala.

20. Ndipo Mose ndi Aroni anacita monga momwe Yehova adawalamulira; nasamula ndodo, napanda madzi ali m'nyanjamo pamaso pa Farao, ndi pamaso pa anyamata ace; ndipo madzi onse a m'nyanjamo anasanduka mwazi.

21. Ndi nsomba za m'nyanjamo zinafa; ndi nyanjayo inanunkha; ndipo Aaigupto sanakhoza kumwa madzi a m'nyanjamo; ndipo munali mwazi m'dziko lonse la Aigupto.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 7