Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 6:18-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Ndi ana amuna a Kohati ndiwo: Amramu ndi Izara, ndi Hebroni, ndi Uziyeli; ndipo zaka za moyo wa Kohati ndizo zana limodzi ndi makumi atatu kudza zitatu.

19. Ndipo ana amuna a Merai ndiwo: Mali ndi Musi. Amenewo ndiwo mabanja a Levi mwa kubadwa kwao.

20. Ndipo Amramu anadzitengera Yokobedi mlongo wa atate wace akhale mkazi wace; ndipo anambalira Aroni ndi Mose; ndi zaka za moyo wa Amramu ndizo zaria limodzi mphambu makumi atatu kudza zisanu ndi ziwiri.

21. Ndi ana amuna a lzara ndiwo: Kora: ndi Nefegi, ndi Zikiri.

22. Ndi ana amuna a Uziyeli ndiwo: Misayeli, ndi Elisafana, ndi Sitiri.

23. Ndipo Aroni anadzitengera Eliseba, mwana wamkazi wa Aminadabu, mlongo wace wa Nasoni, akhale mkazi wace; ndipo anambalira Nadabu ndi Abihu, Eleazara ndi ltamara.

24. Ndipo ana amuna a Kora ndiwo: Asiri ndi Elikana, ndi Abiasafu; amenewo ndiwo mabanja a Akora.

25. Ndipo Eleazara mwana wa Aroni anadzitengera mkazi wa ana akazi a Putieli akhale mkazi wace, ndipo anambalira Pinehasi. Amenewo ndi akuru a makolo a Alevi mwa mabanja ao.

26. Omwewo ndiwo Aroni ndi Mose amene Yehova ananena nao, Turutsani ana a Israyeli m'dziko la Aigupto mwa makamu ao.

27. Awa ndi omwewo ananena ndi Farao, mfumu ya Aigupto, awaturutse ana a Israyeli m'Aigupto; Mose ndi Aroni amenewa.

28. Ndipo kunali, tsiku limene Yehova ananena ndi Mose m'dziko la Aigupto,

29. Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti, Ine ndine Yehova: lankhula ndi Farao mfumu ya Aigupto zonsezi Ine ndizinena nawe.

30. Koma Mose anati pamaso pa Yehova, Onani, ine ndiri wa milome yosadula, ndipo Farao adzandimvera bwanji?

Werengani mutu wathunthu Eksodo 6