Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 6:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yehova ananena kwa Mose, Tsopano udzaona comwe ndidzacitira Farao; pakuti ndi dzanja lamphamvu adzawalola apite, inde ndi dzanja lamphamvu adzawaingitsa m'dziko lace.

2. Ndipo Mulungu ananena ndi Mose, nati kwa iye, Ine ndine YEHOV A:

3. ndipo ndinaonekera Abrahamu, Isake ndi Yakobo, Mulungu Wamphamvuyonse; koma sindinadziwika kwa iwo ndi dzina langa YEHOV A.

4. Ndipo ndinakhazikitsanso nao cipangano canga, kuwapatsa dziko la Kanani, dziko la maulendo ao, anali alendo m'mwemo.

5. Ndamvanso kubuula kwa ana a Israyeli, amene Aaigupto awayesa akapolo; ndipo ndakumbukila cipangano canga.

6. Cifukwa cace nena kwa ana a Israyeli, Ine ndine Yehova, ndipo ndidzakuturutsani pansi pa akatundu a Aaigupto, ndipo ndidzakulanditsani ku ukapolo wanu; ndipo ndidzakuombolani ndi dzanja lotambasuka, ndi maweruzo akuru;

7. ndipo ndidzalandira inu mukhale anthu anga, ndipo ndidzakhala Ine Mulungu wanu; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu, wakuturutsa inu pansi pa akatundu a Aaigupto.

8. Ndipo ndidzakulowetsani m'dziko limene ndinakweza dzanja langa kunena za ilo, kuti ndilipereke kwa Abrahamu, kwa Isake ndi kwa Yakobo; ndipo ndidzakupatsani ilo likhale lanulanu; Ine ndine Yehova.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 6