Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 39:2-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Ndipo anaomba efodi wa golidi, lamadzi, lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.

3. Ndipo anasula golidi waphanthiphanthi, nalemba nsambo, kuti amuombe pamodzi ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, nchito ya mmisiri.

4. Anapangira efodi zapamapewa zolumikizana; pa nsonga ziwirizo anamlumikiza.

5. Ndi mpango wa efodi wokhala pamenepo, wakummanga nao unali woombera kumodzi wa ciombedwe comweci; wa golidi, ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa; monga Yehova adauza Mose.

6. Ndipo anakonza miyala yasohamu, yogwirika m'zoikamo zagolidi, yoloca ngati malocedwe a cosindikizira, ndi maina a ana a lsrayeli.

7. Ndipo anaiika pa zapamapewa za efodi, ikhale miyala ya cikumbutso kwa ana a Israyeli; monga Yehova adamuuza Mose.

8. Ndipo anaomba capacifuwa, nchito ya mmisiri, monga maombedwe ace a efodi; ca golidi, lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.

9. Cinakhala camowamphwa; anaciomba capacifuwa copindika; utali wace cikhato cimodzi, ndi kupingasa kwace cikhato cimodzi, cinakhala copindika.

10. Ndipo anaika pomwepo mizere inai ya miyala; mzere wa odemu, pitida, ndi bareketi, ndiyo ya mzere woyamba.

11. Ndi mzere waciwiri wa nofeki, safiri, ndi yahalomu.

12. Ndi mzere wacitatu wa lesemu, sibu, ndi akalama.

13. Ndi mzere wacinai wa tarisisi, sohamu, ndi yasefe; inakhala yogwirika ndi golidi maikidwe ace.

14. Ndipo miyalayi inakhala monga mwa maina a ana a Israyeli, khumi ndi awiri, monga mwa maina ao; ngati malocedwe a cosindikizira, yonse monga mwa maina ace, kwa mafuko khumi ndi awiriwo.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 39