Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 39:14-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Ndipo miyalayi inakhala monga mwa maina a ana a Israyeli, khumi ndi awiri, monga mwa maina ao; ngati malocedwe a cosindikizira, yonse monga mwa maina ace, kwa mafuko khumi ndi awiriwo.

15. Ndipo anapangira pacapacifuwa maunyolo ngati zingwe, nchito yopota ya golidi woona.

16. Anapanganso zoikamo ziwiri zagolidi, ndi mphete ziwiri zagolidi; naika mphete ziwirizo pa nsonga ziwiri za capacifuwa.

17. Ndipo anamanga maunyolo awiri opota agolidi pa mphete ziwiri pa nsonga za capacifuwa.

18. Ndi nsonga zace ziwiri zina za maunyolo awiri opotawo anazimanga pa zoikamo ziwiri, nazimanga pa zapamapewa za efodi, m'tsogolo mwace.

19. Ndipo anapanga mphete ziwiri zagolidi, naziika pa nsonga ziwiri za capacifuwa, m'mphepete mwace m'katimo, pa mbali ya kuefodi.

20. Ndipo anapanga mphete ziwiri zagolidi, naziika pa zapamapewa ziwiri za efodi pansi pace, pa mbali yace ya kutsogolo, pafupi pa msoko wace, pamwamba pa mpango wa efodi.

21. Ndipo anamanga capacifuwa pa mphete zace ndi mphete za efodi ndi mkuzi wamadzi, kuti cikhale pa mpango wa efodi, ndi kuti capacifuwa cisamasuke paefodi; monga Yehova anamuuza Mose.

22. Ndipo anaomba mwinjiro wa efodi, nchito yoomba ya lamadzi lokha;

23. ndi pakati pace polowa mutu, ngati polowa pa maraya ocingirizira, ndipo anabinyira pozungulira polowa pace, pangang'ambike.

24. Napangira pa mkawo wa mwinjiro makangaza a lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.

25. Ndipo anapanga miriu ya golidi woona, napakiza miriu ndi makangaza, pa mkawo wa mwinjiro pozungulira, popakiza ndi makangaza.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 39