Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 38:12-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Ndi pa mbali ya kumadzulo panali nsaru zocingira za mikono makumi asanu, nsid zace khumi, ndi makamwa ace khumi; zokowera za nsici ndi mitanda yace yasiliva.

13. Ndi pa mbali ya kum'mawa, kum'mawa, mikono makumi asanu.

14. Nsaru zocingira za pa mbali imodzi ya cipata nza mikono khumi ndi isanu; nsici zace zitatu, ndi makamwa ace atatu;

15. momwemonso pa mbali yina: pa mbali yino ndi pa mbali yina ya cipata ca pabwalo panali nsaru zocingira za mikono khumi ndi isanu; nsici zace zitatu, ndi makamwa ace atatu.

16. Nsaru zocingira zonse za pabwalo pozungulira zinali za bafuta wa thonje losansitsa.

17. Ndipo makamwa a nsici anali amkuwa; zokowera za nsici ndi mitanda Iyace zasiliva; ndi zokutira mitu yace zasiliva; ndi nsici zonse za pabwalo zinagwirana pamodzi ndi siliva.

18. Ndi nsaru yotsekera pa cipata ca pabwalo ndiyo nchito ya wopikula, ya lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa; utali wace mikono makumi awiri, ndi msinkhu wace mu kupingasa kwace mikono isanu, yolingana ndi nsaru zocingira za pabwalo.

19. Ndi nsici zace zinali zinai, ndi makamwa ace anai, amkuwa; zokowera zace zasiliva, ndi zokutira mitu yace ndi mitanda yace zasiliva.

20. Ndi ziciri zonse za cihema, ndi za bwalo lace pozungulira, nza mkuwa.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 38