Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 35:24-35 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

24. Yense wakupereka copereka ca siliva ndi mkuwa, anabwera naco copereka ca Yehova; ndi yense amene kwao kunapezeka mtengo wasitimu wa ku macitidwe onse a nchitoyi, anabwera nao.

25. Ndi akazi onse a mtima waluso anapota ndi manja ao, nabwera nalo thonje lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.

26. Ndi akazi onse ofulumidwa mtima ndi luso anapota ubweyawo wa mbuzi.

27. Ndi akuru anabwera nayo miyala yasohamu, ndi miyala yoti aiike kuefodi, ndi kucapacifuwa;

28. ndi zonunkhira, ndi mafuta akuunikira, ndi mafuta odzoza, ndi cofukiza za pfungo lokoma.

29. Amuna ndi akazi onse a ana a Israyeli amene mitima yao inawafunitsa eni kubwera nazo za ku nchito yonse imene Yehova anauza Ipangike ndi dzanja la Mose, anabwera naco copereka cofuna mwini, kucipereka kwa Yehova.

30. Ndipo Mose anati kwa ana a Israyeli, Taonani, Yehova anaitana, ndi kumchula dzina lace, Bezaleli, mwana wa Uri, mwana wa Huri, wa pfuko la Yuda;

31. ndipo anamdzaza ndi mzimu wa Mulungu, ndi luso, ndi nzeru, ndi cidziwitso, za m'nchito ziri zonse;

32. kulingirira nchito zaluso, kucita ndi golidi, ndi siliva, ndi mkuwa;

33. ndi kuzokota miyala voikika, ndi kuzokota mitengo, kucita m'nchito ziri zonse zaluso.

34. Ndipo anaika m'mtima mwace kuti alangize ena, iye ndi Aholiabu mwana wa Ahisama, wa pfuko la Dani.

35. Amenewo anawadzaza ndi luso lamtima, lakucita nchito ziri zonse, ya kuzokota miyala, ndi ya mmisiri waluso, ndi ya wopikula ndi lamadzi ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ndi ya muomba, ya iwo akucita nchito iri yonse, ndi ya iwo olingirira nchito yaluso.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 35