Amuna ndi akazi onse a ana a Israyeli amene mitima yao inawafunitsa eni kubwera nazo za ku nchito yonse imene Yehova anauza Ipangike ndi dzanja la Mose, anabwera naco copereka cofuna mwini, kucipereka kwa Yehova.